Reads: 356

."SOLO! EMILY CHONDE USALORE AFEEEEEEEEEEEEE EEE!!" uku kunali kukuwa kwa Alicia yemwe amayesa kuti ndiine amene ndaombeledwa. Ndinamukuwila kuti ndili moyo koma zinthu sizili bwino. Mmene amatulukira pa balaza nkuti ine ndikudumpha pa window kuti ndikamuone Emily. Zinali zowawitsa zedi kumuona ali magazi okhaokha! Ndinamunyamula ndikukuwa, "Nooooooooooooo! Mayi a Isobar tadzukani! Nooooooooooooo! Siungafe chonchi Emily! EEEEE- MIIIII-LYYYYYYY!!!!! aaaaaahhh!" ndimalira ndikumulanda mfuti. Ndinayang'ana khamu la a police omwe anali atazungulira nyumbayi. Ndinaigwila mfuti ija ndikudzuka mwaukali, "Mkazi wangayu akangofa ndithana ndi nonsenu." ndinatero mopanda mantha ndipo apolice aja anakhonzekeretsa mifut yao yomwe inachita kulira kuti KHOLOKHOTCHO!! Ndinafuna kuti ndiombere koma Billiat anandigwila pamkono, "Solo, tipange kaye zo tipulumutse moyo wa madam'wa bwa??" adandiuza akundilanda mfut uja pang'onopng'ono. Billiat amadziwa kuti akanapanda kundidekhetsa, ndikanatha kuchita zambiri zoopsa. Iye anali ataberekera kachikwama kake kakuchipatala ndipo ananyonyomala ndikuyamba kumuthandiza Emily. Wamkulu wa apolice'wa anatiuza kuti timukweze Emily mgalimoto ndipo tizimuthandiza tikupita kuchipatala. Anatiuzanso kuti nditsale kuti akambirane nane koma ndinawauza kuti tizikambirana mgalimoto mommo. "Solo, mkazi wanu'yu wasanduka munthu woopsa kwabasi! Sabata yokhayi, wapha athu atatu ndipo tangotsimikiza kumene kuti anatuma mzimayi wina kuti akamumalizitse Millias yemwe ali kuchipatala koma mwamwayi sizinatheke." adayamba motero Supretendent Khamula. "Tinalandilanso uthenga kuti anabwera kuno ndikudzaba mwana ndip..." ndinawagwira pamkono ndikuwadula mawu, "Mwanayo ndi wanga. Pezani chifukwa china." Ndinawauza. Iwo anandiyang'ana kenako adaseka, "Ndi zoonadi kuti chikondi ndi chakhungu. Ukukanika kuona kut mkaziyu ndi chimbalangondo??" adafunsa."Mukut anthauza chani??" ndinawafunsa. "Tatiye titsike kaye." adatero akutsegula chitseko poti tinali titafika kuchipatalako. "Solo, dzulo anamwa tameki koma mwachisomo, anatengeredwa kuchipatala. Mmene amatsitsimuka anapeza kut apolice akumufuna mot anamenya dotolo ndikumuvula kenako iyeyo nkuvala zovala zaudotolozo! Pothawa anathawa atanyamula mankhwala amadzi mabotolo atatu komanso ma jekiseni angapo. Solo, mkazi'yu ndikukhulupirira kuti bongo wake wabalalika ndipo akuyenera kuthandizidwa mwachagu wamva??" adandifunsa. Ndinangogwedeza mutu ndikuwatsanzika kuti ndikufuna ndikalowe naye Emily mchipatalamo. *** Ndinathamangira pa bed lomwe anamugoneka nkumamukhukhuluza wokalowa mchipatala. Ma nurse angapo anali jijiri jijiri koma onse anamusiya Emily pomwe wina anakuwa, "Guys, wapha Doctor V.Mwale uja ndi ameneyutu!" Billiat anaitana a police omwe anamuthandiza kukankha bed'li ndikulowa nalo mchipatalamu. Tili mu corridor, ndinangoti gululu ndi Lerato yemwe anali atangotulutsidwa kumene mchipatalamu. "Solo, ndan wagonekedwa pa bed'yo??" Anandifunsa: ndipo ndidaynkha mwachangu, "Mkulu wako!" PHWAAAA! Ili linali mbama la 2KGs lomwe anandiponyera nditangotchula ( olo ndili ine mnakakumenyan5 kgs cz panopa sukudziwa mkazi yemwe ukufuna Solo ndaona ) Iye anatsonya ndikumapita koma mai ake anaima. Iwo anayamba kulira ndipo anatilondola. Titafika ku room imene amafuna kukamuthandizirako, anatiuza kut titsale panja. Ndinawahaga mai ake a Lerato ndikuwauza kuti akhazikitse mtima pansi. "Solo, ndiika bwanj mtima pansi mwana wanga ali mwa kayakaya?? Ndikanakhala kuti sindinamuthawe mwina bwenzi pano asali chimbalangondo chonchi. Chowawitsa nchoti mng'ono wake naye pang'ono ndi pang'ono akusanduka chigawenga chifukwa cha mkwiyo wapa m'bale wakeyu." Anatero mai Kumwenda akugwetsa msozi. Ndinawanvetsa ndipo ndinawauza kuti asadziweruze okha poti iwo siolakwa. Ndinacheza nawo pang'ono kenako Ndinawatsanzika. *** Ndinatuluka muchipatalamu ndipo ndinakumana ndi Alicia yemwe anali atangotsika kumene mgalimoto ya Billiat. Anandiuza kuti ndimudikire ndipo adathamangira mchipatala kukakumana ndi Billiat. Sup. Khamula anali ali panja pom'paja ndipo anandiuza kuti ngati Emily angapulumuke, akafikira kumangidwa ndikuzengedwa milandu. Ndinawayang'ana koma ndinakanika kuwayankha mwano poti amayakhula modekha komanso anali wooneka kuti anali munthu wa nzeru zake. Anali wamfupi, wonenepa wakamimba kake ndithu. Anali woyera moyepula komanso anali ndi mpata mmano awo akumanzere. Ndinaseka kenako ndinawayankha, "Mukungopanga ntchito yanu bwana. Mukuonetsetsa kuti chilungamo chiyende ngati madzi." Ndinawauza ndikuwapatsa mkono ndipo anandiyamikira kuti ndawamvetsetsa. "Sol..." .... "Ndikupitatu bwanawe." Ndinayankhula iwo akufuna aziyankhula. "Mumafuna munene kuti chani?" ndinawafunsa koma anangoti palibe. Ndinamulondola Alicia yemwe anatuluka akulira. "Solo, ndikungofuna kucheza ndi munthu panopa... Billiat ali busy nde chonde chonde tatiye tipite kumalo a phee tikacheze." Anandigwila pamkono uku akundiyang'ana monvetsa chisoni. Ndinavomera ndipo ndinayamba kupita komwe kunali galimoto ija koma anandiuza kuti tiyenda wapansi. *** Tinayenda kamtunda ndithu akungolira. Ndinamutengera ku Chichiri Meseum ndipo tinakafatsa pamalo ena a zii. "Solo, tiye tizicheza tikuyendayenda." Anatero ndipo ndinaimilira. "Solo, ndiwe mnyamata wosangalatsa ndipo ndikutha kumvetsetsa chifukwa chomwe Emily amapangira zonsezi." Anatero."Haha watero?? Koma tiye tiiwale zinazo,,,Tiye ticheze nkhani zathu!" Ndinamuuza. "Solo, sindinganame, Emily ndimangomutenga ngati sister wanga. Kunena zoona, munthu uja anayamba kukukonda kalekale moti kukuyalutsa mclass muja ankapanga ati pofuna kukuthawitsira ma hope haha!" Anaseka akupuputa misozi. Ndinamuyang'ana kenako Ndinamufunsa chomwe amafuna kwa ine. "Solo, ndikufuna timuthandize Emily. Ubongo wake wadzadza ndi mkwiyo poti sanakwanilitse zonse zimene ankafuna. Amafuna banja labwino limodzi ndi iweyo. Ndikukumbukira tsiku lake loyamba kupha; tsiku limene anamupha Gladys lija ukukumbukira kuti anangotuluka mclass osalowanso??" Anandifunsa Ndinavomera ndi mutu ndipo anapitiliza, "Tsiku limene lija ankafuna kudzimangilira!"anapumila, "ndinamulimbitsa mtima kuti asadziphe poti amanyamula mwana wako ndipo chongomuuza choncho anataya tameki wake... Solo, ukudziwa kuti mwana waiwe ndi Lerato anakamusiya kwa agogo ake??" Anaponya funso londidzidzimutsa. "Wati chan?? Chifukwa chan??" Ndinamufunsa. "Eeeh eeh! Tadekha Solo... Amaopa kuti iyeyo sangathe kusamala mwana. Poti mwana uja ndi wako, iye sakanatha kumupha nde anakangomutula kwa agogo ake...Koma chimodzi, tandiuze nchifukwa chani Emily amakamba kuti akufunitsitsa atapepesa kwa Lerato??" Anafunsa ndipo ndinamudziwitsa kuti Lerato ndi mng'ono wake wa Emily. Iye analira poti anati' anathandizira pa udani wa awiriwa. Ndinamuhaga ndikumuuza kuti aiwale zimenezo. Tinacheza pang'ono kenako tinauyamba ulendo obwerera kunyumba kwa Alicia ndi Billiat uja. Ndinamuuza Alicia kuti ndikufuna kukumana ndi mai anga kaye nde tinapita kuchipatala kuja ndikukatenga galimoto wautali ku Chilomoni. *** Ndinangofikira kutsegula gate ndikukalowa mnyumba. Iwo atandiona anandithamangitsa koma ndinawauza kuti sindinabwerere nkhondo. "A Mum, Emily anaomberedwa ndi a police nde panopa ali mchipatala. A Police anena kuti akangotsitsimuka amangidwa kuti aka..." Ndinakanika kupitiriza poti mai anga anali akupumira mmwamba! "Solo, Emily wanditchula?????" ***


Submitted: July 13, 2016

© Copyright 2021 Chiyamiko isobar chiusiwa. All rights reserved.

Chapters

  • Facebook
  • Twitter
  • Reddit
  • Pinterest
  • Invite

Add Your Comments:


Facebook Comments

More Romance Books

Other Content by Chiyamiko isobar chiusiwa

Book / Mystery and Crime

Short Story / Mystery and Crime