MADZI AKATAIKA

Reads: 2292  | Likes: 0  | Shelves: 0  | Comments: 0

More Details
Status: In Progress  |  Genre: Romance  |  House: solo series

Chapter 4 (v.1) - Solo akadali ndi chikondi pa Lerato??

Submitted: July 08, 2016

Reads: 184

A A A | A A A

Submitted: July 08, 2016

A A A

A A A

"TATULUKA MNYUMBA MWANGA MUNO MWACHANGU!" Anamukuwira mphaka yemwe adali atalowera pa window. Emily adamuthamangitsa mphaka uja kenako adamuyandikira Millias uja, "Ukupezako bwanj lero??" adamufunsa ndipo iye adayankha ali chigonere kuti bolako. Ndinafuna ntasunthira pafupi koma Emily adandipsinyira diso kuti ndisatero.

"Kodi wabwera ndi munthu??" Millias adafunsa ndipo Emily adakana. Millias adaoneka olusa kwabasi ndipo adamufunsa Emily, "Mmesa unandilonjeza kut ubwera ndi Solo?? Ndisaname, zomwe zidachitika zija zimandikhudzabe mpaka pano ndipo ndisadafe ndimafuna kut Solo andikhululukire." adamufotokozera Emily kwinaku akubuula. Msozi udagwa mmaso mwanga ndipo ndidakanika kudziletsa koma kumuyandikira ndikumulimbitsa, "Amwene ndakukhululukilani." ndidamuuza ndikumugwira mkono.

Iye adamwetulira pakundiona ndipo anandiuza kuti ngati kuli kotheka, ndimukhululukire Lerato. Ndidamuuza kut ndidamukhululukira kalekale. "Koma ukudwala chan??" ndidamufunsa Millias yemwe adandiyang'ana ndikundipatsa yankho loduka, "Kubwera kwako kwachiza mabala anga." adatero.

"Millias tanena chilungamo!" uyu adali Lerato yemwe adatsegula chitseko cha room'yi. Ndidafuna kumupatsa mbama koma Emily adandiletsa. Lerato adandiyang'ana mmaso kenako anatulutsa mawu, "Solo, tsiku lija unasamuka mu room muno walikumbuka??" adandifunsa ndipo ndidavomera. "Ukukumbukira kuti udamukankha Millias yemwe adagwera pa timagalasi tosweka ta tambula yake??" Atafunsa kachiwirika, ndinakanika kuyankha koma iye anapitiriza, Timagalasi tina tidamulowa kunsanaku ndipo zikuopsa kut akhoza kutaya moyo wake. Apapa akumakanika kuima olo kukhala pansi poti msana wake ukumamuwawa...Tinaimbira akwawo ku Rumphi koma mpaka pano sadapereke thandizo lilironse moti chipitileni naye kuchipatala tsiku limene lija, sitidapitekonso. " adatsindika Lerato.akundiyang'ana ndi diso la chiweruzo.Ndida tulutsa phone ndikuwadziwitsa mai anga za izi ndipo anandiuza kuti abwera kudzamuona Millias. Ndinalira kwambiri poti ndinamupweteka mzangayu ndikuchoka osabwereranso. Ngakhale ndinamupanga chonchi, iye sanandikwiyire ndipo mmalo mwake anafunitsitsa kut ndimukhululukire. Tinakhala mphindi zingapo tisakuyankhulana ndipo Emily anadzuka mwachipongwe, "Solo, tasuntha ndikufuna ndikhale ndi mahope angawa. Iweyo tapita kuli akazi ako Lerato'ko!" Adatero akumugwira mkono Millias yemwe ankangoseleulana kuti mahope. Ndinamugwila pamkono ndikutuluka naye panja. "Usiye kutchukitsa kuti ndife chibwenz wamva??" ndidamuchenjeza ndipo mmalo mwake anatulutsa misozi, "Solo ukanadziwa mmene ndimakukondera sukanatero wamva?? Inetu sindimadziwa kalikonse komanso Millias sanali bwinobwino. Utangochoka muja, Millias anadandaula mmimba ndipo anagona. Patatha mphindi zingapo, nane ndidayamba kumva zachilendo mthupi mwangamu moti mmene ndidapezekera pa bed ndi iye muja sindimadziwa." adalongosola ndi nkhope yokhulupirika koma zinali zondivuta kukhulupirira.ndinamuuza kuti sindingakhulupirire koma iye anakakamila ndipo pang'ono ndi pang'ono ndinayamba kumukhulupirira poti zomwe amakambazo zimafanana ndi mmene ndinanvera tsiku lija nditapita kukalasi kuja. Ndidamuyang'ana kenako mwachisoni, ndidamuhaga. Ndidatseka maso ndipo mtima wanga unali uli kutali, sindimamvetsa kuti ndahoda Mkazi yemwe ndakhala ndikufunitsitsa atakhala wanga!

Tili mkati mohagana, ndidangomva phwaaa! Mbama limene ndidalizindikira kuti limachokera kwa mayi anga. Ndinamukankha Lerato uja ndikutembenuka,

"Iwe, ine kuliza hutala iwe osamva?? Mkazi uyu nde utinso uyu?? Iii basi undiyankhabe, Millias ali kut??" Anafunsa mai anga ndipo ndidawalondolera mu room muja. Titangolowa tidapeza Emily akumukissa Millias ndipo ndinagwira pakamwa kuli kudabwa kumeneko; Choyamba ndimadabwa kuti kodi anthuwa ndi chibwenz?? Chachiwiri kunali kuganizira kuti kodi mai anga ati chani poganizira muja anatipezera panja muja??? Iwo anakhala ngati sanaone ndipo anangofikila kumufunsa Millias momwe amapezera kenaka adamutengera kuchipatala. Titakamusiya kuchipatala, ndinabwerera ku room kwanga kwa tsopano kuja ndipo ndinakamupeza mzanga waku college of Medicine uja, dzina lake Billiat, atangofatsa kuonera filimu yazofufuzafufuz a.Ndinangofikira kumufotokozera Billiat zomwe anandiuza Lerato zija zokhudzana ndi tsiku lama scandal lija. Iye anandiuza kuti akhoza kundithandiza ndipo anandiuza kuti ngati kuli kotheka, ndimupititsire ka chakudya olo kachidutswa ka chakudya chimene ndinalandira cha mu lunchbox chija. Ndinamuuza kut ndikayang'ane kaye ndipo anandiuza kuti andidikira. Ndinabwerera ku room kwa Millias kuja apa nkuti nthawi ikuyandikira kut ikwane 7:00 ya usiku. Nditafika uku, ndinangofikira kutsegula poti mmene timapita ndi Millias kuchipatala, anandisiyila ma key. Ndinasuzumila chipinda chija ndipo mwamwayi, ndinapeza chi carton cha lunchbox chija ndipo munali tizinyenyeswa ta chakudyacho. Ndinatenga carton'yi ndiku yamba ulendo wobwerera koma nditangotuluka, ndinapeza mtsikana wina akundidikira. Ndinamuunika ndi foni ndipo ndinapeza kuti anali mmodzi mwa atsikana awiri omwe ndinakawapeza class tsiku lija. Ndinamufunsa chomwe amafuna ndipo anati tilowe kaye mu room muja.Ndinaseka ndipo ndinamuuza kuti ndizosatheka. Iye anandiuza kuti pali chomwe amafuna kundiuza ndipo ndinavomera kuti tilowe. Titalowa, iye anandiuza kuti ali ndi uthenga ofunikira koma andiuza tikagonana kaye. Ndinamuuza kuti zimenezo ndimasungira m'banja ndipo iye adaseka, "Hahahahaha Solo uli serious?? Nanga tsiku lijali unkakatani ku Hostel ya atsikana?? Koma Solo iweyo ndi Moreen! Mmesa unathana ndi akazi awiri tsiku limene lija??" Anandifunsa ndipo ine ndinangoti zii kusowa choyankha. Ndinayesera kukumbukira mmene ndinakafikira ku hostel ya atsikana tsiku lija koma sindimakumbukira. Chomwe ndimakumbukira chinali choti ndili class, ndinayamba kumva kupepuka komanso kuti munthu wina adandinyamula koma sindinamuone. Ndinadziwa kut zitha kutheka kuti atsikana ena ake anandigwilirira. Ndikufuna ndizifunsa funso lina, ndinanva kugogoda ndipo kusuzumira pa window, ndinaona kuti anali mayi anga omwe anakuwawo, "Solo ndikudziwa kuti uli ndi mkazi mmenemo koma tatsegula mwana wanga ine sindichedwa!! ****************************** Kodi mai ake a Solo amadzatani ku room kwa Millias'ku usiku ngati umenewu?? Mukuganiza kuti mtsikana/atsikana omwe anamuchita chipongwe akhoza kukhala ati komanso chifukwa chani?? ********** PressNext ShareThePost


© Copyright 2018 Chiyamiko isobar chiusiwa. All rights reserved.

Chapters