MADZI AKATAIKA

Reads: 2471  | Likes: 0  | Shelves: 0  | Comments: 0

More Details
Status: In Progress  |  Genre: Romance  |  House: solo series

Lerato amangidwa poganiziridwa mlandu wakupha...Solo wabalalika ndipo alandira uthenga wina wobalalitsa...

Chapter 5 (v.1) - Lerato ndi wokupha??

Submitted: July 09, 2016

Reads: 232

A A A | A A A

Submitted: July 09, 2016

A A A

A A A

"SI ZIMENE MUKUGANIZAZO AMAYI!!" Ndinawauza ndikukatsegula. Iwo atangolowa, anagwila pakamwa poti anampeza mtsikanayu atayamba kuvula. "Solo, mkazi winanso??" Anafunsa Mayi anga ndi mtsikana uja anatsonya ndikukokera malaya ake ndikutuluka mokwiya. Ndinawayang'ana mayi anga omwe anayamba kundilangiza zokhudzana ndi AIDS... Amazikonda izi nthawi zambiri akamandilangiza zazibwenzi moti kwa ine idafika poti nkhaniyi inali itanditopetsa. "WABADWIRA KWA DOTOLO SAOPA KUMVA ZAMATENDA!" ndimadziuza ndekha mumtima. Iwo atamaliza kundilangiza, anayalura blangete la Millias ndikunditsanzika, "Mzako uja sakupeza bwino moti wagonekedwa pa Queens pompa apa." adatero ndipo ndinangowauza kuti ayende bwino. Atapita, ndinangotuluka ndikuloka chitseko cha room ija basi ndi kumapita ku room yanga ya tsopano ija. Ndinamupatsa Billiat zotsalira za lunchbox ija ndipo anandiuza kuti mawa apita nazo ku sukulu kuti akaziyeze. Ndinazikakamiza kugona usiku umenewu ndipo movutikira momwemo, ndinagona. Mawa lake kutacha, ndinapita ku sukulu ndipo ndinalawirira ndithu. Ndinapezapeza mtsikana uja anandigwila naye dzulo uja akucheza ndi Lerato. Ndinamuyang'ana kenako ndinapita kumbuyo kukakhala. Lerato atandiona, anabwera ndikuzandipatsa moni ndipo anandipempha kuti ndikapeza mpata ndipite naye ku chipatala masana kukamuona Millias. Ndinavomera pongofuna kumusangalatsa ndipo iye anandiuza kuti ndimukhululukira pa mbama yomwe mai anga anandipatsa atandipeza nditahagana naye. Diso langa linamuphethilira ndipo iye anangoseka. Titamaliza kuphunzira, ndinapita naye kuchipatala komwe tinauzidwa kuti Millias akupeza bwino ndipo mmasiku ochepa akhala akutulutsidwa. Uku tinachokako mochedwa kenako tinapita pa chiwaya kukadya kanyenya.Nkhani zinabulika mpaka kunja kunada tikudyabe kanyenya. Titamaliza, iye anandipempha kuti ndimuperekeze poti amaopa kunja komwe kunali mdima wokhawokha. Ndinalora poti ndinalinso ndi zochita zina ku hostel ya atsikanayi. Ndinakamusiya pa room pake ndipo ananditsanzika ndi kiss. Nditangosiyana naye, ndinazemba ndikupita kwa Gladys, mtsikana amafuna kugona nane dzulo uja. Ndinapita osati kuti ndikakwanilitse zomwe amafunazo ayi, koma kuti ndikamunyengerere ndi ndalama kuti andiuze zomwe amafuna kundiuzazo. Ndinamugogodera ndipo iye anatsegula akuyasamula. "Ii sorry ndakudzutsa!" Ndinamuuza koma iye ananseka ndikundiuza kuti ndilowe. Nditalowa, iye anandiuza kuti amalota ine ndi iyeyo titakwatirana. Ndinaseka koma anandiuza kuti ali serious ndipo maloto ake ndi amenewo. Ndinamufotokozera chomwe ndinabwerera koma anandiuza kuti sakufuna ndalama zanga, ndikufuna thupi lako, mtima wako komanso chikondi chako!" Anatsindika. Ndinamuyang'ana kenako ndinamunyengelera, "ngati ukufuna zimenezo, yamba kaye wandiuza atsikana omwe ndinagona nawo tsiku limene lija komanso ngati ukumudziwa amene adanditumizira lunchbox." Ndinkamuuza izi ndikumumwetulira ndi cholinga choti ndimukomedwetse koma mmalo mondimvera, adangoyamba kuvula. Ndinayesetsa kumuletsa koma ayi sananinve. Phone yanga inaitana ndipo nditayankha? Anali mayi anga. Nditawapatsa moni, chitseko chinatsekulidwa ndipo Lerato anatulukila, "Asa! Gladys mamuna wanga ukutani naye??" Anafunsa ndiye kuti ine ndili pa phone pamenepa. Mai anga anandifunsa chomwe chimachitika koma ndinangoidula phone'yo. Lerato anatenga pillow wa Gladys ndikundimenya naye pamutu! Kenako anamupatsa mbama Gladys.ndinamul ongosolera kuti si mmene akuganiziramo koma iye sanayankhe. Lerato ananena kuti wandikhulupirira koma analonjeza kuti athana ndi Gladys. Ndinayesera kumulankhula koma iye anandikhalitsa chete nde paja ukagwa m'mbuna suyankhula, ndingokhala phee! Anatenga pillow wa Gladys ndikumugendera kenako anandigwila mkono ndikundiuza kuti tipite ku room kwake. Ndinangovomera posafuna kulakwitsa zinthu ndipo titapita uku, ndinamupatsa zomwe ndimakana kumupatsa Gladys zija. Ndisaname, Lerato ndinamukonda kuposera aliyense. Ndinagona ku room kwakeko moti ndimachokako chamma 4 koloko mmawa. Ndinakafika ku room kwanga komwe ndinakangofikira kusamba ndikumapita ku sukulu. Billiat anandiuza kuti andiuza zotsatira ndikachoka kusukulu. Ndinasamba mwachangu ndikuuyamba wakusukulu. Nditalowa, Emily anabwera kudzandihaga ati kundilandira ndipo ndidangosekerera ngat zilibwino. Lerato anabwera ya nyumwitsa ndikundikissa. Emily anafuna kupanganso zomwezo koma ndinamukanira ndipo anthu anamudzuma. Iye anangotuluka ndipo sanabwererenso. Kalasi ili mkati, kunatulukira a police, "Tikufuna Lerato Soko." datero kuwauza aphunzitsi athu. Iwo anamuloza Lerato ndipo apolice anamuuza atuluke. Ndinatuluka naye limodzi ndipo a police anati akumufuna kuti akayankhe mafunso awiri atatu okhudzana ndi imfa ya Gladys Kumwenda. Tonse tinadabwa ndipo ndinawafunsa a police chomwe amatanthauza, "Gladys wamwalira?? Nthawi yanji komanso wafa ndi chani??" Ndinafunsa modabwa poti usiku wadzulo ndi uja tinali limodzi uja. Wa police wina anandiyang'ana kenako anayankha, "Wamwalira kamba kobanika. Zikusonyeza kuti kumupha kwake, anamuvindikila ndi pillow. Msungwana wina yemwe anamupeza atafa ndi amene anadzanena ndipo tauzidwa kuti dzulo, munthu womaliza kulowa mu room yake anali Lerato'yu!" adatero akumutenga. Ndinawauza kuti ndinali naye limodzi koma anakana kundimvera ndipo mmalo mwake anangoti abweranso nthawi ina.Ndinangolowa class ndikunyamula mabuku anga komabe anthu anandikakamila kuti ndiyankhulepo. Ndinawadziwitsa kuti Gladys Kumwenda waphedwa ndipo Lerato Soko chibwenzi changa ndi amene akuganiziridwa koma siolakwa.Ena anakhulupilira koma ena anakana kukhulupirira mumadziwa inu sionse amakondwa. Madzulo tsiku limenelo anandidziwitsa kuti pillow wa Gladys wapezeka ndi ma fingerprint a Lerato. Ndidayesera kuwatsimikizira kuti zoonadi Lerato anagwira pillow'yo koma sizinali zoti anamugwira pokupha ayi komabe boma linakana izi. Patapita mwezi umodzi, Lerato Soko anamugamula kukakhala kundende kwa zaka 27... Tsiku limene ankagamulidwa, linali tsiku lomwe Millias ankatuluka mchipatala. Tsiku limeneli linandibweretsera zambiri poti Billiat naye anandiululira zotsatira za kuyesa kwake kuja, "Solo, zakudya zomwe zinali mu lunchbox yomwe unalandilayo, zinathilidwa Cubatixis hT30 (not real) yemwe apangitsa kut munthu uzifuna kugonana. Mankhwalawa amayamba kugwira ntchito pakatha mphindi 29..." Nditamva izi, ndinakamupepesa Millias poti ndinadziwa kuti sanali olakwa. ***zzzz_ Panadutsa sabata imodzi, Emily anabwera ku room kwanga. Iye anabwera akusekerera ndipo adatulutsa chi pepala chomwe anaika mu envolope ndikundipatsa. Nditangowerenga ndinadzidzimuka kwabasi. "Iwe uli...?????" *zz******** Mukuganiza kuti Lerato anali olakwa?? Ngati ayi, anapha Gladys ndani?? Chifukwa chani??


© Copyright 2019 Chiyamiko isobar chiusiwa. All rights reserved.

Chapters

Add Your Comments: