MADZI AKATAIKA

Reads: 2283  | Likes: 0  | Shelves: 0  | Comments: 0

More Details
Status: In Progress  |  Genre: Romance  |  House: solo series

Chapter 8 (v.1) - kwabadwa mapasa...

Submitted: July 12, 2016

Reads: 169

A A A | A A A

Submitted: July 12, 2016

A A A

A A A

"KODI MA HUG SACHITIKA APA?? AAAA KOMA ALICIA!" adafunsa Emily ndipo tonse tinaseka. Iye anamuhaga Billiat ndipo ine ndinamuhaga Alicia. Atandihaga, anandinong'oneza kukhutu, "Chilichonse chobisika chiululika pompano. Ungodekha." adatero ndipo ndinaseka. Emily ananena kuti tipite tikadye malo amodzi ndipo tonse tinavomera monyinyirika. "Kodi munakumana bwanji??" Emily anamufunsa Billiat tikudikira kuti chakudya chathu chibwere. Billiat anaseka kenako mkuyankha kuti, "Haha mkazi'yu ndimamudziwa ndikale kungoti sukulu inkandipatsa busy nde sindinkakumana naye. Miyezi iwiri yathayo ndiimene ndinatsitsa mfundo ndipo anandilora." Ndinaseka ndipo ndinafunsa funso ngati sindikudziwa, "Bro, paja dzina lija umati ndiwe ndan??" "Billiat..." adayankha. "Okay Billiat, umakhala kutiko and unkaphunzira kuti??" ndidafunsa ndipo iye anandiyankha. Chakudya chinabwera ndipo tinadya ndipo titamaliza, tinatsanzikana. Emily anamuitana Alicia pambali ndipo ndinapezerapo mpata wokambirana ndi Billiat, "Kodi mukusewera iti iti??" ndidamufunsa. "Solo, nditapita kukamuona Lerato masiku am'mbuyomu, anandionetsa zithunzi ndipo nditaziona, ndinayang'anitsitsa kuti kodi wojambulayo anaima pati ndipo nditaunguzaungu za ndidapeza kuti anali Alicia." adayamba kufotokoza choncho uku akusuzumira ngati anthu akumumva. "Owo??" ndidamufunsa modabwa. "Inde amwene Solo!" Anandiyankha ndipo anapitiliza, "ndinamusaka saka mtsikanayu koma sindimamupeza. Lero mwamwayi ndinakumana naye ali kuchipatala nde ndinamukakamira moti anaulura kuti anajambula ndi iyeyo koma amati sangaulure yemwe amamutumayo poopa kuti akhoza kuphedwa ngat mmene..." anadukiza kenako anapitiliza, "ngati mmene adaphedwera Gladys." Ndinadzidzimuka koma ndinakanika kufunsa poti atsikanawa anatulukira, "Muzichezatu!" Anatero Emily. Alicia anaoneka wa nkhope yakugwa ndipo anapempha kuti azipita.Emily anamuhaga Billiat ndikumutsanzika, "Mula uyende bho." ***zzzzz*** Ndinasiyana ndi Emily ndipo Ndinapita ku room kwanga komwe ndinakamupeza Millias akuwerengera ndalama. Nditangotsegula, anaoneka otangwanika kubisa ndalama ndipo ndinakhala ngati sindinamuone. Ndinangoziponyera pa bed panga kenako ndinazivindikira ndi pillow. "Amwene Thuso Paipi ndi chan??" adafunsa akuseka ndipo anandiitana pa dzina lomwe anthu adandipatsa kumpira. "IiiiiiiIi kodi uli mommuno et??" ndinayankha ngati kuti sindinamuone. "Simunandione man?? Emily yemweyu ameneyi??" Anaseka uku akutseka chikwama chomwe anaikamo ndalama zija. Ndinadzuka ndikukhala pansi kenako ndinasendera pomwe Millias anakhala, "kodi aise, ku ukwati kuja unkafuna undiuze kuti chani??" Ndinamuponyera funso. Iye anakanda mmutu kenako mkuseka, "Aaa man inali nsanje mukudziwa mkazi uja ife timamufira." anayankha zomwe sizinandigwile mtima. "Ndinu abale athu, mukudziwa?? Tangonenani man." ndinayesera kumunyengerera koma mau omwe anandiyankha adandiopsa. "Nthawi zinazake ndi bwino kukhala mbuli pankhani zinazke ndi cholinga choteteza moyo." Anatero uku akunyamula chikwama chake nkumapita. Ulendo umenewo anabwerako madzulo ndipo anandipeza nditangokhala pa bed uku ndikuganizira chomwe chimachitika. Iye anandpepesa koma anandiuza kuti moyo wanga amaukonda ndipo sanganene kuopa kuti ndizikhumudwa. Mawu amenewa ndinawalingalira kwakanthawi koma sindimatha kupezamo yankho. Masiku anathera kuchitseko ndipo tsiku lina, Emily anandiuza kuti ndimuperekeze ku sikelo (scale). Monga mwini mwana, Ndinapita komko ndipo tinachitika mwai kuti kunali anthu ochepa. Ndinakhala panja pampanda kumudikira Emily ndipo mwamwayi, Billiat anatulukira ndinamupatsa moni. Anandifotokozera kuti pazifukwa zina, iyeyo ndi ine tichepetse kucheza pafupipafupi. Ndinamufunsa ngati panali chomwe ndinalakwa koma ananditsimikizira kuti zonse zili bwino.Ndinamuyang'ana koma poti ndimamudziwa bwino, ndinangovomera poti ndimadziwa kuti chilipo chomwe akukonza. Atangochoka Billiat, kunatulukira Emily yemwe anandiuza kuti zonse zili bwino. Poti sindinali sure, Ndinamufunsa kuti mimba inali ya miyezi ingat ndipo anandiuza kuti yakwana miyezi 5 tsopano. Ndinasangalala kuti mmiyezi yochepa ndikhala ndikutchedwa bambo a uje! *** [3 Months later/Patapita miyezi itatu] *** Ndinali ndili class pomwe thenifolo yanga inalira ndinatuluka panja kukayankha. Oimbayo anali Emily koma sitimanvana ndiye ndinangobwerera kukalowa mkalasi. Nditalowa, phone ya Alicia inalira ndipo iye anatulutsa kuona, inali message atangowerenga, anakuwa akusekerera, "YES!! HAHA Solo ndi Lera... Ooh Solo ndi Emily tsopano!" Anakuwa moteromo. Ndinadzidzimuka ndi zomwe amakambazi ndipo ndinamuponyera funso kuti akutanthauzanji. "Solo, Emily wabereka mapasa; Wammuna ndi wamkazi. Congrats my dear!" Anatero ndipo anthu anaombera mmanja ena mpaka kumamenya matebulo. Aphunzitsi nawo anandiombera mmanja ndipo anaseleura anvekere ndawaposa poti iwo anali ndi mwana mmodzi. Titasokosera kwa mphindi ndithu, anthu anakhala zii pomwe anaona kuti sindikuoneka osangalala. Millias anasuzumira pa window ndipo adakuwa, "Thuso paipi 2 goals! kkkkkk congrats bro!" Atangonena izi phokos linayambiranso ndipo mtima wanga unayamba kuthamanga. Ndinatuluka ndikumwetulira uku anzanga akungokuwa, "Solo! Solo!" Ndinatengana ndi Alicia yemwe anati akufunitsitsa atakhala mmodzi mwa anthu oyamba kunyamula ana anga. Tinatengana wakuchipatala ndipo titafika uku, ndinakumana ndi Billiat yemwe anandiyamikira, "Bambo a mwana tsopano!" Ndinaseka ndipo ndinamukonza, "Bambo a ana! Olo ukhoza kumangoti bambo a 'tiwiri' kkkkk" ndinatero tsopano nditatsimikizika kuti siinali ntchedzero. Ndinalowa mchipinda momwe munali Emily'mo ndipo ndinangofikira kumupatsa kiss, "Wandipatsa tanthauzo la moyo wanga SoMily..." Ndinamutchula dzina lophatikiza maina athu. "Solo, apapa banja timalota lija latheka basi..." Anadukiza pomwe anaona kuti nkhope yanga yasintha.Mawu amene anayankhula oti "...BANJA TINKALIFUNA LIJA..." Anandikumbutsa malonjezano omwe ndimkapatsana ndi Lerato aja. Ndinafuna kukhetsa msozi koma ndinaona kuti zidzetsa mafunso osayankhika. Koma poti msozi subwezeka, unatuluka mwamakani. Pofuna kuphiphilitsa nkhani, ndinanyamula tiana tanga tamapasato ndikuyankhula, "ndinakapanda kuvomera mimbayi mwina bwenzi nditakupangitsa kuti utaye ana awiri... Zikomo poti unandilimbikitsa Emily!" ndinatero ndikumumwetulira Emily mwabodza ndipo kankhope kake kanawala moti anasekelera. Nane ndinasekerera kuti bodza latheka. Posakhalitsa, bambo ake a Emily anatulukira mchipindamu limodzi ndi mai anga.Iwo analowa atanyamula shawelo ziwiri zapamwamba kwabasi. Mayi anga anatiyang'ana kenako anatenga phone yawo ndikumupatsa Alicia. "Tatijambule!" adatero akuwakokera bambo a Emily pa bed pomwe panali ine ndi Emily. Bambo anaoneka osakhutira ndi izi komabe adangopanga momwemo. Alicia anatiuza kuti akujambula ndipo chodabwitsa chinali choti mai anga anakoloweka mkono wawo mnkhosi mwa bambo a Emily. Chithunzi chachiwiri, iwo anawatsamila bambowa. Tikuti tizijambulitsa chithunzi china, bambo anaimilira ndikutuluka. Emily anaoneka okhumudwa koma atayang'anizana ndi mai anga, anasekelera ndipo anahagana. **** Patatha sabata imodzi, ndinafatsa mu room mwanga limodzi ndi Millias yemwe amaoneka obalalika kwabasi. Iye anauzidwa kuti anapita kundende ndipo anauzidwa kuti akaidi ena sakuoneka. Anandiuza kuti Lerato ali mgulumo. Ndinanjenjemela ndipo ndinamutsanzika Millias kuti ndikupita kukamuona. Ndinanyamuka nditafika uku, adandiuza kuti tsiku limene anasowa Lerato, mu cell yake munapezeka magazi ndipo akaidi anzake anati sadziwa chomwe chidachitika poti iwo anali akugwira ntchito ya kalavula gaga. Ndinabalalika ndi zimene ndinauzidwazi ndipo ndinabwerera kuti ndizipita ku room kwanga. Nditangotuluka mumpanda wa Chichiri prison, ndidamva munthu kundiitana pa galimoto ina yomwe inali pafupi ndi galimoto yanga yomwe bambo a Emily anandipatsa. Monyinyirika Ndinapita kuti ndione kuti ndindani . Atangotsegula chitseko, munthu'yo anandigwila pakamwa ndikundilowetsa mgalimotomo. Munthu wina yemwe anavala mask anatuluka mgalimotomo ndikukakwera mgalimoto mwanga. Vvuuumu! magalimoto onse anayamba kuyenda... ***** Kodi anthu omwe amugwira Solo akhoza kukhala ndan?? Kodi mukuganiza kut Lerato adafa?? Kapena chinamuchitikila ndi chan?? Nanga nchifukwa chani mai a Solo amawagwira bambo a Emily mwa chikondi??


© Copyright 2018 Chiyamiko isobar chiusiwa. All rights reserved.

Chapters

Add Your Comments: